You're welcome to MalawianCameras
YouTube Channel Here we do these things
Reactions
News updates and commentary
Fun videos
Vlogging
So feel free to interact with with us
We need your wisdom and support
Let's build the world together with love and respect and peace
Malawian Cameras
Jomo wangopepesa basi kuti zithe😂.
Mfumu ya mzinda wa Blantyre Isaac Jomo Osman wabwera poyera ndikuvomereza zomwe zili mkanema wina yemwe akuonetsa iye akupanda khofi mai wina.
Izi zikutsatira kusamvana komwe kunabuka pakati pa Osman ndi mai-yu yemwe amam'ganizira kuti amagula katundu obedwa.
Zitachitika izi, boma komanso mabungwe ndi nthambi zina zinabwera poyera ndikudzudzula mchitidweu.
Koma kudzera mu kalata yake, Osman wati wavomereza kulakwa kwake kaamba koti anachita zinthu zosemphana ndi udindo wake.
"Ndikufuna ndinene kuti zomwe ndinachita sizoyenera..." Yatero kalatayo.
Malingana ndi kalatayo, ndi udindo wa mfumu ya mzinda kuwonetsetsa kuti anthu akukhala motetezeka, molemekezedwa komanso umoyo wabwino.
Pakadali pano, Osman wati, "ndine odzipereka pa kafukufuku aliyense pa nkhaniyi komanso kupepesa kwa 'mama'".
3 weeks ago | [YT] | 149
View 45 replies
Malawian Cameras
#Times360Malawi
Yemwe anali nduna ya za Chuma a Simplex Chithyola Banda amangidwa ndi apolisi (Fiscal) lero.
Malinga ndi lawyer wa a Chithyola a Jivason Kadzipatike kumangidwa kutsatitira chikalata (Warrant of arrest)chomwe chinatengedwa ku bwalo la Mkukula.
Pakali pano apolisi sananene chomwe awamangira. A Chithyola akadzipereka okha ku polisi.
By Mercy Matonga
1 month ago | [YT] | 96
View 12 replies
Malawian Cameras
Moni ndine Jackie walemba izi
Iran yasiya dziko liri kukamwa kakasu.
Chikhalire, zimadziwika kuti ali ndi ma misayilo ofika 2500km.
Nde mayiko ena amadalira ma base omwe ali kutali poti ma misayilowa sangafikeko.
Koma ma misayilo awili anaponyedwa ulendo wa 4000km. Kupita ku base ina ya amelika ku Diyego Garcia.
Anthuwa akusunga ma joker anji
2 months ago | [YT] | 227
View 29 replies
Malawian Cameras
Dzulo tinati mphekesera zosezi zitha Netanyahu akabwera live ndipo 1 hour ago wabwera live
Kusonyeza kuti alimoyo Gulukunyinda khakhakha ameneyu
Ubwino wake ife takhala tikukana kuti tinene nkhani yoti tilibe nayo umboni n'chifukwa sitinanene nao zoti wafa
Zikomo
2 months ago | [YT] | 127
View 80 replies
Malawian Cameras
Jackie walemba izitu
Ndikanakhala advisor nkanati ayi musayambe nkhondo ndi awa.
Ngakhale mu history, gulu ili siligonja ndipo siliwopa kufa.
Liri ndi history yayikulu, nthawi inayake inali empire yamphamvu dziko lonse.
Ndi okuti amakakamila olo agendedwe bwanji, mpaka umangotopa wekha..
Pano zikuvuta kuyituluka kwake.
It's not about uli ndi mbali. Koma anthu anali phee kupanga zawo achita kuwayamba.
Bruce Lee anati..
Never underestimate your opponent.
2 months ago | [YT] | 404
View 59 replies
Malawian Cameras
#Malawi24
#Nkhani
Nyuzipepala yaikulu m'dziko la United States, ya CNN, yatulutsa report limene lawulura kuti dzikolo likufuna kupereka upangiri komanso zida za nkhondo ku gulu lotchedwa Kurdish ndicholinga cholanda dziko la Iran.
Malinga ndi nyuzipepalayi, dziko la America lipanga zimenezi kuti gulu la Kurdish lidzimenyana ndi asilikari a dzikolo, zomwe zipangitse kuti mu Iran mukhale magulu angapo ankhondo omwe agonjetse asilikari a Revolution Guard Corps, kwinaku akulanda boma nkulipereka kwa anthu.
Izitu zikudza pomwe malingaliro a Donald Trump ofuna kusintha ulamuliro wa dzikolo utaomba khoma kamba kakuti ataphedwa Ayatollah Ali Khamenei, dzikolo silidachedwe koma kusankha Ayatollah Alireza Arafi ngati mlowam'malo kuti pasakhale njira yomwe ikhonza kubweretsa chisokonezo m'dzikomo.
Ndipo nyuzipepalayi yatsimikiza kuti sitepe yotsatira yomwe dziko la America yapanga ndi kulimbikitsa gulu la Kurdish kuti limenye nkhondo ya pansi, kwinaku likugawa malire omwe apangitse asilikari a dziko pa Israel ndi America kulowa mosavuta m'dzikomo.
Anthu amene apatsidwe upangiriwi ati mpata umene wapezeka osintha kayendetsedwe ka dziko la Iran ndi unowu ndipo angodikira dziko la America kuti litumize asilikari ake omwe aphunzitse guluri maphunziro a ku nkhondo komanso kupereka zida zamakono zomwe agwiritse ntchito pofuna kusokoneza dziko la Iran.
Pakadali pano, kumenyana pakati pa Iran ndi maiko a Israel komanso America kukupitilira pomwe mizinga ikusinthana mulengalenga.
Maiko a Israel ndi America agwira kakasi kamba kakuti samayembekezera kuti nkhondoyi ifarikira ku Middle East konse ndipo amayembekezera kuti nkhondoyo sidutsa masiku oposa anayi.
2 months ago | [YT] | 80
View 22 replies
Malawian Cameras
Beautiful People
Magetsi azimilatu kuyambila mamawa nde koma nkhani tikutolera
Akayaka ma update ose abwera ndithu
Stay safe out there!!!!!
Malawian Cameras
2 months ago | [YT] | 100
View 22 replies
Malawian Cameras
Good Morning!
Kanema wa dziko la Iran walengezano zakuphedwa kwa Supreme leader wa Iran Ayatollah Ali Khamenei
Kwalamulidwa kuti pakhale masiku 40 olira maliro
Utsogoleri ukupitilirabe
Mau amkuluyu anali oti tose tidzafa ife tidzafera mom'muno kutikwiliraso mom'muno tisingathawe......
Malawian Cameras
2 months ago | [YT] | 187
View 61 replies
Malawian Cameras
Trump komaso Nyumba zoulutsira nkhani zaku Israel zatsimikiza kuti Supreme leader wa Iran Ayatollah Ali Khamenei waphedwa
Ngakhale kuti Dziko la Iran silinatsimikize za Nkhani yi
Ma ola 4 apitawo Nduna ya Iran yowona zakuja Abbas Araghchi inafusidwa pa CNN kuti Ali Khamenei alimoyo kapena ai iye anayankha kuti alimoyo pamodzi ndi akuluakulu enaso ali safe
Kotero Sitikudziwa kuti Zoona ndiziti,koma ngati zili zoona izo anakonzekera kale that's why anasankhiratu Alowa m'malo ake kusonyeza kuti Kuphedwa kwa Iye sikuntha kwankhondo
Apa tidikira ma report otsimikizika ochokera ku dziko la Iran
USIKU WABWINO
Stay Safe
Malawian Cameras
2 months ago | [YT] | 53
View 16 replies
Malawian Cameras
Apolisi atsimikiza zoti amanga nduna yakale yoona chitetezo cha m'dziko a Ezekiel Ching'oma.
Poyankhula mneneli wa nthambi yapolisi m'dziko muno a Lael Chimtembo ati akhale akufotokoza munthawi yake zifukwa zomwe awamangila a Ching'oma.
Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.
4 months ago | [YT] | 80
View 6 replies
Load more